Mankhwala a m'chilengedwe-Dr.phiri

Mankhwala a m'chilengedwe-Dr.phiri INO NDI PAGE YA DOCTOR PHIRI MWINI PROGECT YA HOCEDA HERBS, NDIMAPHUNZISA KOMANSO KUGULISA MANKHWALA chinsinsi chozama Cha mankhwala amchilengedwe

ZOONA ZA MITUNDU YA MKODZO WANUCHOLINGA cha phunziroli ndicho kuti tizidziwa zoyenera kuchita tikadabwa NDI mkodzo wathu...
28/09/2025

ZOONA ZA MITUNDU YA MKODZO WANU

CHOLINGA cha phunziroli ndicho kuti tizidziwa zoyenera kuchita tikadabwa NDI mkodzo wathu chifukwa pena imakhala Vuto lalikulu lomwe likuyamba mwa inu Nde dziwani Izi musanawerenge za mitundo ndalembayi:

Chithunzi chili m'munsichi chikuonetsa mitundu yomwe ndatchulayi mundondomeko yogwirizana kuyambira pa 1 mpaka 10.

Mukamawerenga pa nambala inayake muzisuzumiranso pa nambala yofananayo mu chithunzi Kuti muzimvesa zomwe ndikutamthauza.
Tagwilizana eti!!!Nde tiyeni sopano::::::

1. Mkodzo wopanda mtundu ulionse (clear urine) ndi chizindikiro chosonyeza kuti munthu wamwa madzi wochuluka kwambiri.

2. Mkodzo wooneka wa kachifunga (pale transparent) ndi chizindikiro chosonyeza kuti munthu wamwa madzi okwanira.

3. Mkodzo wachikaso choti bii (dark yellow) ndi chizindikiro chosonyeza kuti munthu sakumwa madzi okwanira.

4. Mkodzo wa mtundu wa olanje (orange) ndi chizindikiro chosonyeza kuti munthu sakumwa madzi okwanira.
** Ma vitamini ena komanso kumwa mankhwala ena kumachititsanso mtunduwu pa mkodzo.

5. Mkodzo waolanje woti bii/bulauni (dark orange/brown) ndi chizindikiro chosonyeza kuti munthu sakumwa madzi okwanira. Nthawi zina chimakhala chizindikiro cha vuto la chiwindi/mphafa (liver problem).

6. Mkodzo wabulauni wa bii kapena wokuda (dark brown or black) ndi chizindikiro chosonyeza kuti munthu ali ndi limodzi mwa mavuto awa: vuto la chiwindi, kuvulala kwa minofu (rhabdomyolysis), kusagayika kwa mchere wokulitsa wa pulotini; m'Chingerezi protein (alkaptonuria)

7. Mkodzo wapinki kapena wofiira (pink or red) ndi chizindikiro chosonyeza kuti mumkodzomo muli magazi. Nthawi zina zimakhala zotsatira za zinthu zomwe mwadya kapena mwamwa, monga beetroot.

8. Mkodzo wamtundu wa madzi (blue) kapena wobiriwira (green) zimakhala zotsatira za kudya zinthu zosinthira makaka a zakudya (dye, used for food colouring). Koma wobiriwira ungathenso kusonyeza mavuto a m'chikodzodzo.

9. Mkodzo wa mtundu wa mtambo (cloudy) ndi chizindikiro chosonyeza mavuto a njira ya mkodzo (urinary tract infections)

10. Mkodzo woyera kapena wa mtundu wa mkaka (white or milky) ndi chizindikiro chosonyeza kuti madzi ochokera m'mitsempha otchedwa 'lymph' amene amanyamula zakudya (nutrients) akudonthera mu impso, ndipo amasakanikirana ndi mkodzo. Vuto limeneli limatchedwa 'chyluria'.

Muli ndi zotupa mchiberekeroMunapangidwa opareshop koma siikupolaMuli ndi vuto la miyendo akutupa mpaka kukanika kuyenda...
27/09/2025

Muli ndi zotupa mchiberekero

Munapangidwa opareshop koma siikupola

Muli ndi vuto la miyendo akutupa mpaka kukanika kuyenda

Muli ndi chilonda chosanva mamkhwala

Muli ndi opareshop yomwe siikupola

Muli ndi vuto la dzino

Munachosedwa dzino nde chilonda chikuwawa

Muli ndi zilonda pa mulomo kamba ka edzi kapena kutsika kwa chitetezo

Muli ndi zilonda kukhosi

Mwauzidwa kuti muli ndi vuto linalake likufuna opareshop

Muli ndi vuto linalake mchiberekero kapena khansa

Panopo zatha simukachekedwa mukangomwa chitsamba ichi chomwe chikupezeka mu Hoceda herbs Basi

Trancagem ndi mankhwala omwe atha kukonza mavuto onsewa mosavuta ndipo kusintha mukuona kuyanbila tsiku mwayamba kumwalo

Chitsambachi chimagwila ntchito monga njira yopulumukira pa mavuto aakulu omwe afika pothesa mzeru KU chipatala
Samalani Pali zitsamba zambili zofanana ndi trancagem ndipo zimapha koma Pali chitsamba chimodzi chokha chomwe chimachita kulimidwa sichipezeka Mtchile kapena paliponse mtaunimu
Mukafuna kupewa mavuto aakulu aja omwe munauzidwa kuti mukhala nawo moyo onse gulani trancagem mu Hoceda herbs kunena zoona muzathokoza
Ngakhale khansa imagonja ndi trancagem kokha mukufunika kutsatira kametedwe kake mpaka miyezi 6

Tridax procumbensMankhwalawa amapanga chilichonse chomwe diclofinac,panado ngakhale aspirin atha kupanga Koma popanda ku...
27/09/2025

Tridax procumbens
Mankhwalawa amapanga chilichonse chomwe diclofinac,panado ngakhale aspirin atha kupanga Koma popanda kubwereramso mavuto ena
Chitsambachi chimathandiza pá matenda a shuga,khansa,edzi,zizonono,madzi KU ndata,no mpaka mavuto a Mu imphsyo
Kapamgidwe kake mkosavuta kungoidula ngati ndiwo mkuyeza supuni imodzi ya mankhwala mkuika mkapua ya 150ml mkuzaza madzi otemtha mkutakasa mkubindikira,zikazizila mkusefa mkumwa
Mupamge Izi katatu pa tsiku
Yeserani simuzakhumudwa

Ngati simutha kupeza chitsambachi panokha itanisani mankhwala kudzera pa watsap yathu titumiza kuchokera KU mozambique KU Tete komwe kuli chipatala chathu chá na herbs

18/04/2025
Ena amandifunsa aphiri Kodi pangapezeke mtengo omwe paokha utha kuthesa mtundu ulionse WA matenda?Mwachidule ndiyankhe k...
18/04/2025

Ena amandifunsa aphiri Kodi pangapezeke mtengo omwe paokha utha kuthesa mtundu ulionse WA matenda?
Mwachidule ndiyankhe kuti mitemgo ndi yambili yali ndi mphanvi yomweyi koma mtengo umodzi osavuta kupeza omwe utha kupanga chilichonse mukufuna ndi thonje

Eya simunanve molakwika ndikunena za thonje amene mumamudziwa uja
Inuyo kupeza thonje ndiye kuti Muli ndi chipatala pakhomo palibe matenda angakanike ndi thonje
Mungofunika kupanga tiyi basi supuni imodzi ya mankhwala Mu kapu imodzi ya madzi otentha akazizizla musefe mumwe
Mupamge Izi katatu o patsiku
Mmmmm aphiri mwanena kuti matenda onde nde ngati ndi vuto lá pakhumgu momga ziphuphu ndi zilonda?eya simunalakwe ndanena kuti matenda onse nde zimakhala ziphuphu kapena zilonda tsukirani kapena sambani ndi tiyi yemweyu

Chosangalasa ndi choti ndinachilisapo matenda a água munthu wina pomgogwilisa ntchito masamba ndi mizu ya thonje
Maluwa ake ndimawagwilisa ntchito kwanbili pa azimai omwe AMAVUTIKA mmimba akamasamba
Koma ndanena kuti chilichonse ndi mankhwala nde samalani pa mafuta a nthanga za thonje ndi kulela WA azibambo moto kungomwa kamodzi Muli ndi tsiku lathunzu uma wanu sungapase mimba mzimai
Nde mmalo mokhaulisa azimai ndi kulera onyansa WA mzipatala inuyo azibambo imwani mafuta ya thonje nanunso mulereko asaaaa kumangonzunza azimai eti!

20/01/2025

KU LILONGWE TAPEZA SHOP KU AREA 49 MOTI MWEZI WA MAWA TITSEGULA MA HERBS ATHU KU LILONGWE

ndinapempha kuti mutithandizeko kupeza ka shop kakamgono ku lilongwe ndi ku blantyre titsegule shop yathu ya ma herbs ku...
06/01/2025

ndinapempha kuti mutithandizeko kupeza ka shop kakamgono ku lilongwe ndi ku blantyre titsegule shop yathu ya ma herbs kuli ziiii

Kuonjeza pakukonza kuti umuna ukhale okhota bwino komamso kuteteza mimba kuti isachoke therere limakuza tsitsiKuti zithe...
06/01/2025

Kuonjeza pakukonza kuti umuna ukhale okhota bwino komamso kuteteza mimba kuti isachoke therere limakuza tsitsi
Kuti zitheke pangani chonchi
Dulani dulani therere Itatu muike mbale muike kapu imodzi ya madzi,siyani kwa hora limodzi,mukatero sefani tikufuna madzi okhota aja nde thirani mmadzimo supino imodzi ya shuga ndi imodzi ya mafuta a ntsatsi sakanizani ikani mu mankhwala any aja atsitsi otchedwa shampoo kunena zoona muzandothokoza pa zotsatira za tsitsi lanu

06/01/2025

Minba yanu imangochoka?
Pezani therere lobala muchose nthanga zakezo kenako mukazimge musinje mupamge ufa muzimwa ngati Tiyi kawili pa tsiku
Supino imodzi mu kapu ya madzi otemtha
Mumwe kwa miyezi Itatu minha yanu siizachokanso mdipo simuzabalila kumpeni

Si zokhazo nanunso azibambo ngati uma wanu si okhota bwino komamso mphanvu zakuchipinda mzochepa pangati Tiyi omwewu

*Thesani vuto losowa magazi lero*Tikuluza achibale ambili kamba kosowa magazi nde lero aphiri abwera kuzaulula zinsinsi ...
09/12/2024

*Thesani vuto losowa magazi lero*
Tikuluza achibale ambili kamba kosowa magazi nde lero aphiri abwera kuzaulula zinsinsi zozama za mmene tingathesere vutoli
Chifukwa cha kuchuluka zochita sindikukwanisa kulemba nkhani tsiku ndi tsiku koma musachoke mgulu lino chifukwa apo ndi apo zabwino zizibwera

Mankhwala amphanvu othesera kusowa kwa magazi ndi masamba cabichi kupanga tiyi osakaniza ndi tsabola
Koma ngati mukufuna zachangu kwanbili pezani kalombo komwe pachiputukezi timati catato
Kalomboka sindidziwa kuti mu chilankhulo chanu mumati chani koma ndikuonesani chithunzi
Nde mukufunika kusinja kupanga ufa mkumamwa ngati tiyi ufawo olo kungophika mkumupasa adye odwalayo
Pa masiku atatu okha odwala apeza magazi onse omwe thupi lake likufunikira
Si zokhazo mukapangira odwala matenda ashuga mphanvu ya catato ndi yofanana ndi mapilisi otchedwa metiformin aja amene amakankha shuga kuchosa mmagazi kulowesa mmaselo athupi zikatero munthu amapeza bwino koma vuto la metiformin ndi loti amatsitsa mphanvu za kubedi mpamene catato amaonjeza mphanvu mwa odwala .pali zambili zoti ndikuphunziseni za katato koma mpata ndi ochepa ndizilemba pamgonopamgono chomwe mukufunika kudziwa ndi choti pali catato yemwe amagwa mmakungwa a mtengo woola komanso pali zija zimagwa mmasamba zonse ntchito ndi yofanana
Katato ali ndi ma protein ambili kuposa msomba komanso kuposa nyama ya mgombe katato ali ndi chilichonse chothandiza kuti munthu akhale moyo.

Endereço

Tete

Notificações

Seja o primeiro a receber as novidades e deixe-nos enviar-lhe um email quando Mankhwala a m'chilengedwe-Dr.phiri publica notícias e promoções. O seu endereço de email não será utilizado para qualquer outro propósito, e pode cancelar a subscrição a qualquer momento.

Entre Em Contato Com O Negócio

Envie uma mensagem para Mankhwala a m'chilengedwe-Dr.phiri:

Compartilhar