Health and Healing Products

Health and Healing Products (Timapedzeka ndi mankhwala amatenda onse pamtengo otsika)
Heal the world and build up new body styles

29/04/2026

Shout out to my newest followers! Excited to have you onboard! Willard J Kabango, Bréy NdAh, Joyce Luciano

Takulandirani

Ndi angati amene gas mpaka pano ikuvutabe kuti ithe? Bwerani pano tikambirane imeneyo lero ikutha!
29/04/2026

Ndi angati amene gas mpaka pano ikuvutabe kuti ithe?
Bwerani pano tikambirane imeneyo lero ikutha!

PLANTAGO MAJOR ✓Dzina langa ndine plantago major.✓Ena amangoti "Common plantain."✓Ineyo ndine chomera champhamvu zedi✓Nd...
26/04/2026

PLANTAGO MAJOR
✓Dzina langa ndine plantago major.
✓Ena amangoti "Common plantain."
✓Ineyo ndine chomera champhamvu zedi
✓Ndimathana ndi chifuwa cha mtundu uli wonse.
✓Izitu zimatheka chifukwa ndimasungunura ndi kuchotsa makhololo m'thupi.
✓Ngati mukuvutika ndi chifuwa chosamva mankhwala, chimfine, asthma ndi matenda ena akudza kamba ka kuchuruka makhololo m'thupi ndipezeni
✓Mukandipeza muthyole masamba anga
✓Ndipo muwaphike ndi kumamwa makapu awiri patsiku
✓Mudzitero tsiku ndi tsiku kwa masiku 54. Asthma ndimayigonjetsa.

Zikomo. Ine ndine Common plantain. Ondifuna apeze mbeu ndipo andidzale pakhomo pake. Mukhale ndi tsiku labwino.

25/04/2026

*NJIRA ZOPHERA MWAMUNA UKATOPA NAYE*

```Mzimai wina atatopa nalo banja lake anafuna kungopha mwamuna wake ndipo anapita kwa amayi ake kukafunsa njira imene angamuphere mwamuna wina aliyense popanda wina aliyense kuziwa kuti wachita izi ndi iye.
Ndipo atauuza amai ake anam***andiza motere, mzotheka mwana wanga zomwe ukufunazo koma, ziwa ukuenela kupanga kaye zinthu zoti anthu asakhulupilire kapena kuganiza kuti wachita ndi iwe, nde ukuenela kuchita izi

_💠 Uzimukonda kwambiri mwamuna wako, kuposa wina aliyense.

_💠Usapange zinthu zoti m***a kuyambana nyumbamo kwa miyezi itatu.

_💠 Uzimuchitila nsanje kwambiri.

_💠 Akakupasa ndalama osamanyinyi ngakhale ili yochepa.

_💠 Uzimulemekeza kwambiri.

_💠Usapange zinthu zomuphyesa mtima.

_💠 munthawi ina iliyonse mupase mwachikondi.

_💠Mukamakangana chonde osamakweza mau, ndipo iwe kwako kuzikhala kupepesa basi kuopa kuti anthu angakumvereni kuti mukukangana.

_💠Uzionesesa kuti mtendere ndiumene ukumanga nthenje nyumba mwako.

Ndipo mai anafunsa ukwanisa? mzima anayankha eya ama, ndipo anampasa tiufa ndipo anati uyu ndi tamerc ndipo uzithira muchakudya cha mwamuna wako daily kwa masiku makumi atatu.

Patangodusa makumi atatu mzimai uja anapitaso kwa amayi ndipo anati ama, mwamuna wanga uja wasinthiratu sindikufunanso kumupha chonde pangani zoti tarmec uja asagwirenso ntchito chonde ama, ndikamupha sindizapezanso mwamuna wabwino ngati amene uja.

Ndipo amai aja anaseka, ndipo anati:

kkkkkkk kuterokotu ufa uja sanali tarmec ayi, unali ufa chabe
chimene chimasowekela mwa iwe anali malangizo amene ndinakupasa aja, waona? Mwamunayotu sanasinthe ayi ndi yemwe uja... koma iwe ukumuona kusintha chifukwa iwe mwini wasintha chikhalidwe, mwana wanga banja ndi chikhalidwe, chikhalidwe mchomwe chimapangisa kuti banja likhale lokoma.

Kuyambira lero uzisatila malangizo amene ndakupasa kuti banja likhale lolongosoka```
👫🏾
Mulungu akudalitseni nose

*SOURSOP*~Soursop ndi mtengo wazipatso omwe mulungu adaupasanso machiritso kumatenda osiyanasiyana. Ndipo ubwino wake nd...
25/04/2026

*SOURSOP*

~Soursop ndi mtengo wazipatso omwe mulungu adaupasanso machiritso kumatenda osiyanasiyana. Ndipo ubwino wake ndiochuluka.

*MA UBWINO AKE*

*KUTHANA NDI CANCER ILIYONSE*
~Mphamvu zomwe zili mu masamba amenewa zimapha cancer cells komanso kuchidza matenda amenewa mopanda zovuta komanso mwachangu.

*DIABETES/SUGAR*
~ masamba a soursop amathandiza kwa anthu omwe amadwala sugar kubwenza mmalo mwake.

*KUWAWA KWA NSANA*
~Kupweteka kwa nsana masiku ano ndiyo nthenda yomwe ili mkamwa mkamwa ndipo kubwila mankhwala achipatala kukhadza kuyambitsa mavuto ena pomwe masamba a soursop mulungu adawapasa mphamvu yochidza matendawa popanda kuyambitsa zina nthupi.

*NYAMAKADZI ILIYONSE*
~Nyamakazi ndimatenda omwe amagwila kwambiri azigogo athu koma pano aliyense ikumuzunguza kamba zovuta zina ndipo masamba a soursop ndi mankhwala ake.

*URIC ACID*
~Ngati tili ndi vuto la acid kuti wagwila pena pake mnthupi lathu, Masamba a soursop amathandiza mphamvu ya mulungu.

*KUPANGA BOOST IMMUNE SYSTEM*
~Pedzani masamba a soursop muza booster immune system yanu.

*KUSISA HIGH BLOOD PRESSURE*
~Ngati bp yanu yakwela yesesani kupedza masamba amenewa ndikumamwa ndipo bp yanu izafika pa low penimpeni.

*FEVER*
~Ngati tavutika ndi fever masamba a soursop ndi mankhwala.

*KUTUPA KULI KONSE KWAZIWALO.*
~Fufudzani komwe kuli masamba a soursop mkumamwa.

*KUFEWESA THUPI*
~Mukufuna ka nkhungu kanu kakhale kofewa ndikopanda mabampu?. Pezani komwe kuli masamba a soursop muzigwilisa ntchito.

*KUSAMALA TSITSI*
~Muli ndi tsitsi longonyolozoka ngati mphaka ogwela mu msuko wa thobwa? Inu madando njeee. Fufudzani komwe kuli masamba a soursop.

*KAPANGIDWE KAKE*

*NJIRA YOYAMBA*
~Pezani masamba a soursop a fresh ochulukilapo aikeni mu ntondo ndikusinja kenako aikeni pa saka losukidwa bwino ndi kufinya akwana 1 glass ndipo sakanizani ndi 1 and half glass ya madzi a ginger owirisidwa madzi okhawo basi ndipo Thilani 3 teaspoons ya uchi wa original ndikutakasa bwino lomwe.

25/04/2026

*MATENDA OKHUDZA MTIMA*

*"Kuthana ndi mavuto a mtima."*

*👉 Pali zakudya zanthu zomwe tingazipeze mosavuta zoti zili mu makwalala mwathu momwemu zothetsera mavuto amtima koma kamba kosadziwa timango dzidutsa tiyeni tizione zimenezi👇.
*
👉 Ufa wa masamba a malambe kuika muchakudya .

👉 Muziyika adyo muzakudya zanu muzathandizika kuvuto la mtima.

👉 Kumadya masamba a malambe ngati ndiwo muzathandizika kuvuto la mtima.

👉 Sendani nthochi yaiwisi ndi kudula dula kuyanika ikauma muziika mu cup ya madzi otentha ndikumamwa or muziphika

phala la ufa wa malambe.

👉 Kumadya mtedza osachotsa ka khungwa ka kunja kaja mumapezamo (OPCs) mankhwala awa amathandiza kuchiza mtima, Cancer, ndi Stroke.

👉 Kudya ndiwo zoika maluwa a maungu (chiluwa) muli phytosterols.

👉 Muzikondanso kudya phala la soya.

*CHEST PAIN / KUPWETEKA KWA PA MTIMA*

👉 Tengani tablespoon imodzi ya powder wa adyo kuyika m'madzi ofunda ndikumwa. Kapena mukhoza kungodyaso Adyo wamuwisi ndikumwera madzi.

👉. Imwani ¼ cup ya AloVera juice.

👉. Ikani teaspoon imodzi ya Apple cider vinegar m'madzi ofunda mkumamwa kamodzi patsiku

👉. Tengani ½ teaspoon ya turmeric powder komanso kapu imodzi ya mkaka otentha.

Sakanizani ndikumwa.
👉. Tengani teaspoon imodzi ya ufa wa Cayenne Pepper komanso Tambula imodzi juwisi aliyese wazipatso. Sakanizani ndikumwa.

*KUWAWA KWA MTIMA!*
👉 Tengani teaspoon imodzi ya Unfiltered Apple Cider Vinegar kuphatikiza ndima teaspoon 4 a Uchi wa chilengedwe mu mkapu ya madzi ofunda.
👉Muzimwa kawiri tsiku lililose kwa masabata awiri.

👉 Kuwawa kwa mtima idzakhala mbiri kwa inu.

*"Komano tivetsetsane, tanena kuti (UNFILTERED APPLE CIDER VINEGAR komaso NATURAL HONEY 🍯)"*
Osati bola ali Apple Cider Vinegar ayi.
Osati bola uli Uchi ayi

*KUUMA KWA KHOMO LA CHIBEREKERO (VAGINAL DRYNESS)*Kuuma Kwa khomo la chiberekero kumachitika pamene mkati mwa khomo la c...
25/04/2026

*KUUMA KWA KHOMO LA CHIBEREKERO (VAGINAL DRYNESS)*

Kuuma Kwa khomo la chiberekero kumachitika pamene mkati mwa khomo la chiberekero mukulephera kunyowa. Izi nthawi zina zimachitika chifukwa cha kuchepa Kwa estrogen. Estrogen ndi homoni timene timathandiza kuti mkati mwa khomo la chiberekero mukhale mwa nthazi labwino komaso mudzinyowa mokwanira pamene mkazi akufuna kugona ndi mamuna. Ngati estrogen saturuka okwanira mkati mwa khomo la chiberekero mumanyala ndipo izi zimapangisa kuti mkati mwa khomo la chiberekero mukhale mouma kmaso kutupa
Zifukwa zina zomwe zimapangisa kuuma Kwa khomo la chiberekero ndi kuchotsedwa Kwa timatumba topangira mazira,, kukhumudwa kwambili,, sopo,, mafuta ena odzola,, perefiyumu,, fodya,, mankhwala ena q kuchipatala kmaso ma kondomu amayambisaso vutoli.
*ZIZINDIKIRIO*
1. Kumva kuotcha pokodza
2. Magazi amatha kuoneka pang'ono Mai akangomaliza kugonana ndi mamuna
3. Mai amamva ululu akamagonana ndi mamuna
4. Kuyabwa Kwa khomo la chiberekero
5. Tizilonda mkati mwa khomo la chiberekero
*NJIRA ZA CHILENGEDWE ZOTHANA NDI VUTOLI*

*1. KUSEWERETSANA*. Mkati mwa khomo la chiberekero mukhoza kutenga nthawi yotalikirapo kuti munyowe bwino bwino choncho ndi kofunika kwambili kuyamba ndi kuseweletsa khomo la chiberekero ndi mbali zina monga nkhumbu za mabere musanayambe kugonana
*2.COCONUT OIL.* Kuuma Kwa mkati mwa khomo la chiberekero kumachitika pamene mkati simukunyowa maka maka pamene mukufuna kugonana. Mudzigwiritsa ntchito mafuta a coconut kufewetsa mkati mwa khomo la chiberekero. Mafuta a coconut amathandizaso vuto la mauka
*3. ZAKUDYA ZA SOYA.* Mudzidya kwambili zakudya zopangidwa ndi soya chifukwa muli estrogen
*4. ZIPATSO.* monga mabvembe,, nkhaka,, kmaso Apple
*5. MADZI.* kumwa madzi okwanira pa tsiku kum***andizaso pa vutoli
*6. MTEDZA.* Mu mtedza muli mafuta a bwino omwe amathandiza kuti mkati mwa khomo la chiberekero mukhale mofewa kmaso mudzidya nthanga zomwe zili ndi vitamin E monga nthanga za maungu kmaso za mpendadzuwa

*AZIMAYI OMWE MULI NDI VUTO LA LOW LIBIDO (KUSAKHALA NDI CHILAKOLAKO KUCHIPINDA) KAPENA SIMUMVEKA KUKOMA NDI MAMUNA WANU...
25/04/2026

*AZIMAYI OMWE MULI NDI VUTO LA LOW LIBIDO (KUSAKHALA NDI CHILAKOLAKO KUCHIPINDA) KAPENA SIMUMVEKA KUKOMA NDI MAMUNA WANU*

_*UTHENGA WANU UWU*👇🏾👇🏾👇🏾_

*More fire🔥Moto ku Ndata/Abuja🍑🔥🥰*

*RECIPE I✍🏽📝*

```ndatitu azimayi omwe ali ndi vuto la Low libido (kusakhala ndi ma feelings ku bedroom).```

*Tiyeni tipeze zinthu izi:*👇🏾👇🏾
✅ ```bwemba (chikhatho chimodzi).```
✅ ```Sweet wa Janus uja (10).```
✅ ```ginger wa fresh (zikhawo ziwiri).```
✅ ```madzi 2 litaz.```

*KAPANGIDWE KAKE*👇🏾
➡️ _Tengani bwemba wanu ikani mu mpoto momwe muli madzi 2 litaz aja, zikayamba kuwira ponyani sweet wa Janus 10 uja, kwinaku mukutakasa, kenako tengani ginger oti mwasenda kale wa fresh akhale kuti ndiwosinja ponjanimo zitokotere limodzi pamoto paja uku mukutakasa mwachifatse😃 mphindi 8/12 zikubwata._

➡️ _Kenako phulani nkusefa zinthuzo bwinobwino, sungani madziwo pamalo abwino, mudzimwa madzi amenewo half tambula kawiri patsiku mpaka azathe. M***a kusunga mfiriji mongozizira koma osati mfiriza kuti ziume ayi.._

➡️ _Mukazamaliza kumwa zimenezo dziwani kuti Ndata yanu mwaipatsa moto🍑🔥wachikoka pakakomedwe ku chipinda iLovo iLovo ndithu shuga wachilengedwe tseketseke moto kuti juu mamuna wanu akalowako ku Abujako. Muzamva munthu wabambo kubwebwetuka tima promises pamenepo ntchito ili mkati😅😅._

*RECIPE II✍🏽📝*
➡️ _Phikani masamba amtengo wa bwemba uja, zikawira phulani nkupungura madziwo akwane tambula kenako akhale mphindi 5, inu mayi ponyani ma sweet ajanus atatu mmadzimo takasani zisungunuke zonse zikatero imwani. Inu nthawi yomwezi nyamukani ulendo ku chipinda, kukakhaulitsa mphongo yanu kuli Kukoma eeetu chakwanu leka kuno wabwera banja😅😅👨‍❤️‍👨💋🫂._

*NOTE*
✍🏽📝 ```AZIMAYI SANKHANIPO NJIRA IMODZI YOMWE MUKUONA KUTI M***A KUWANITSA BWINOBWINO (RECIPE I KAPENA RECIPE II.)```

*CHENJEZO⚠️*
*Tsekani pakhomo🚪la chipinda🛌🏼chanu ndi ma key🔑🗝️, ndatitu ndi key🔑🗝️🚪 pameneponso ma window🪟ndithu chifukwa ana angazayambe kudabwa kuti *KODI KULI CHANI🤣🤣🤣

*💱  2026  FIVE ROUNDS CHALLENGE*◀️Kwa omwe sim***a kubwereza Kuchipinda iyi ndi challenge yanu.- Thelele lobala- nthochi...
25/04/2026

*💱 2026 FIVE ROUNDS CHALLENGE*

◀️Kwa omwe sim***a kubwereza Kuchipinda iyi ndi challenge yanu.

- Thelele lobala
- nthochi
- mtedza
. Anyezi ofiila

*Mapangidwe ake*
~ sindinena kukonda zaulere inu🤒.
- *inuyo Kupanga iyi koma osakabwereza Ku chipinda ko mzabweza data yanu🤓*

▶️Munthu unagonja bwino bwino, gadaf wako toothpick koma busy Kupanga makani ndi kuchuluka mzeru.
- munthu sudzuka mokwanira km busy makani .... Kumakhala Kulodzedwaaaa chan❓

🔼 Pali zinthu zina Kumavomereza fast fast ndi bwino...
- ambiri mumati zinthu zake zovuta kupeza....... aaaaa Inu Ku Malawi Kuno kulipo komwe kulibe Thelele lobala, nthochi, mtedza, adyo❓
**

🔻 *Challenge iyi ubwino wake::::::*
- kuthetsa vuto losabereka.
- Kupanga ma round ambiri ( 5 kupita mtsogolo).
- mkazi / mamuna samatopa msanga
• *izi pa tsiku limodzi m***a kugonana ndi akazi atatu onse ma round atatu atatu🤣.*
- umuna umatuluka okhathamira
- umuna umatuluka wambiri.
- Gadaf amafufuma/ amakula bwino mkumakagunda kaja kozuna kaja😆
- gadaf amakhala wa mphamvu
- ndata imanyowa bwino
- ndata siphwisa
- ndata imatuluka ukazi wabwino
- ndata sikhala ndi madzi chuchuchu.
- mkazi amatenga mimba mosavuta.
- mkazi amakhala ndi good shape ( mbina , hip ndi mabere abwino.

👉Dulani Dulani thelere lobala lija ndkusakaniza ndi mtedza kenaka ikani nthochi yanu ija ya fresh yosenda kuidula dula tengani anyezi ofiila ndkudulirako onjezani mchere mulingo wabwino.

Tengani spoon yanu Ndkutakasa yambani Kudya

*Zimakoma ukamazidya kwambiri very sweet ngati thawi yofanana😂*

*Si matenda onse ali matenda enanu mukufunikira munthu akupaseni service yabwino basi osati Mankhwala*

*KUCHIZA MATENDA A BP**REMEDY OF High blood pressure*Choyambilire tidziwe kuti BP ndi nthenda yakuthamanga magazi yomwe ...
25/04/2026

*KUCHIZA MATENDA A BP*

*REMEDY OF High blood pressure*
Choyambilire tidziwe kuti BP ndi nthenda yakuthamanga magazi yomwe imayamba chifukwa chakuchuluka kwa nkhawa (stress) komanso zakudya zina ndi zakumwa zina komanso zifukwa zina

Nthendayi ikakula usinkhu imabala nthenda zina nthupi monga izi👇
1️⃣ kufa kwa ziwalo (stroke)

2️⃣ Dzanzi

3️⃣ Kuphwanya kwa thupi ndikuwawa kwa miyendo

4️⃣ kuwawa kwa mutu pafupi pafupi

5️⃣ kufooka kwa thupi
Ndizifukwa zina

*NJIRA ZOCHIDZIRA NTHENDA YA HIGH BLOOD PRESSURE*
👇👇

1 👉 *KALONJI BLACK SEED OIL*

Pamene mukudwala nthenda ya BP pofuna kuyigonjesa tengani madzi otentha okwana kapu mkuyikamo 1 tea 🥄kalonji ndi 2 tea spoon molinga powder ndi ndi uchi 2 tea spoon ndikumwa ndipo pangani izi kwa miyezi iwiri

2 👉 *Organic Raw unfirutered Apple cider vinegar*

1 tsp ya Uchi ndi 2 tsp za Apple cider vinegar mu cup ya madzi otentha.
Imwani mixture imeneyi kummawa musanadye. Remedy yomweyi imathandizanso ku cholesterol.

3 👉 *Garlic*

Tafunani clove imodz ya garlic m'mimba muli empty, then mwerani madzi glass imodz. Iyi ndi best remedy ya
*high blood pressure*

4 👉 *Papaya*

Idyani papaya kummawa kuli konse musanadye kanthu kwa masiku angapo.

4 👉 *Orange komanso Coconut*

Dulani orange pakati ndikupanga squeeze juice ndikuphatikiza ndi half coconut water.
Imwani half cup ya mixture imene katatu patsiku.

6 👉 *Olive leaves*

Wiritsani masamba 5/6 a olive mulingo wa cup imodz ya madzi kwa 5 minutes yokha.
Imwani cup katatu patsiku.

7 👉 *Mango juice*

Imwani juice wa mango cup imodz, pakatha 1 hour Imwani cup imodz ya mkaka otentha wa fresh, mutathiramo pinch ya cardamom komanso pinch imodz ya nutmeg ndi 1 tsp ya ghee.
Note : ngati muli ndi vuto la sugar ndiye wakwera siyani ghee musagwiritse ntchito.

8 👉 *Okra--Therere lobala*

Dulani Therere lobala kupanga salad ndikumadya .

Address

Lonjezobuleyabanda@gmail. Com
Blantyre

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Health and Healing Products posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Share