03/09/2026
🩺 MATENDA OSAPATSILANA (NCDs)
Matenda osapatsilana ndi matenda omwe samatengera kuchokera kwa munthu wina kupita kwa wina.
Zitsanzo zake ndi:
🩸 Kuthamanga kwa magazi
🍬 Matenda a shuga
❤️ Matenda a mtima
🧠 Stroke
🎗️ Khansa
🫘 Matenda a impso
⚠️ Matendawa amatha kuyamba popanda zizindikiro zoonekeratu. Choncho, musadikire mpaka mutadwala kwambiri.
✅ Muzidya zakudya zopatsa thanzi
✅ Muzichita masewera olimbitsa thupi
✅ Chepetsani mchere ndi shuga
✅ Pewani kusuta komanso kumwa mowa mopitirira muyeso
✅ Muzipita kukayezetsa thanzi nthawi ndi nthawi
Dziwani thanzi lanu. Pewani matenda. Yezetsani msanga.
👉 Tsatirani tsamba lathu kuti mupeze malangizo ena othandiza pa zaumoyo.
🏥 Our Lady of Mt. Carmel Hospital