Mphukira Foundation

Directions Website

Mphukira Foundation A nonprofit organization dedicated to improving lives through education, awareness, prevention, and hope.

Our current focus is kidney health in Malawi and beyond.

25/11/2026

HAPPY BIRTHDAY, HAFEEZ!

Friends who used to hike with the founder of Mphukira Foundation are not stopping at October. They continue to use their passion for hiking to spread kidney health awareness.

Among them is Hafeez Nkhwanda, who, together with his friend Tumpale Mwamomodwe, hiked Michiru Mountain to raise awareness about kidney disease and the importance of protecting our kidneys.

Today, we celebrate Hafeez's birthday and appreciate his continued commitment to spreading the kidney health message.

Happy Birthday, Hafeez! Wishing you many more years of good health, adventure and meaningful climbs. Keep spreading the kidney health message!

Different mountains. One conversation.

Know Your Kidneys. Protect Your Future.

21/11/2026

IMFA ZOBWERA CHIFUKWA CHOSOWA MAFUTA A GALIMOTO

Anthu odwala matenda a impsyo amayenera kupita ku Dialysis kawiri kapena katatu pa sabata, malinga ndi mmene adotolo awalangizira.

Kulephera kulandira dialysis pa nthawi yake kumaika miyoyo yawo pachiswe. Angathe kudwala kwambiri, kutupa miyendo, manja ndi nkhope, komanso kuvutika kupuma chifukwa cha kuchuluka kwa madzi ndi michere mthupi.

Ndiye kodi kusowa kwasokoneza bwanji nkhani ya zaumoyo?

Lero mu program yathu ya PEOPLE WHO KNOW, tikumva nkhani ya Austin Luciano, mnyamata wachichepere amene matenda a impsyo asintha kwambiri moyo wake ndi tsogolo lake.

Onerani nkhani yake kuti mumve kuchokera kwa Austin mwiniwake.

Dziwani za impsyo zanu. Tetezani tsogolo lanu.

20/11/2026

MATENDA A IMPSYO AKHONZA KUFUFUTA TSOGOLO LA MUNTHU.

Austin Luciano anayamba kudwala matenda a impsyo ali ndi zaka 20 zokha, pa nthawi imene anali ndi maloto ambiri okhudza tsogolo lake.

Koma atadwala, moyo wake unasintha kwambiri. Chifukwa chofunika kupita ku dialysis kawiri pa sabata, anayamba kuona ngati maloto ake onse afufutika ndipo tsogolo lake lawonongeka.

Kodi matenda a impsyo asintha bwanji moyo wake? Nanga akukumana ndi mavuto otani?

Loweruka lino, pa 21 November 2026, musaphonye nkhani yonse ya Austin Luciano mu Program ya PEOPLE WHO KNOW pompano pa Mphukira.

Dziwani za impsyo zanu. Tetezani tsogolo lanu.

19/11/2026

KODI KUSOWA KWA MAFUTA KUKUKHUDZA BWANJI ANTHU ODWALA MATENDA A IMPSYO OMWE AMAFUNIKA KUPITA KUCHIPATALA KUKALANDIRA THANDIZO?

Austin Luciano ndi m'modzi mwa anthu odwala matenda a impsyo amene amafunika kulandira thandizo la dialysis pafupipafupi.

Chifukwa cha vuto la kusowa kwa mafuta, kodi akukumana ndi mavuto otani pankhani ya mayendedwe opita kuchipatala?

Loweruka, pa 21 November 2026, tikhala tikumva nkhani ya mnyamata wachichepere, Austin Luciano, mu program ya PEOPLE WHO KNOW.

Dziwani za impsyo zanu. Tetezani tsogolo lanu.

Address

Blantyre
27703

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Mphukira Foundation posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Shortcuts

Share